|
CEFE
- Competency based Economies through Formation of Enterprise
CEFE ndi maphunziro
a anthu ofuna kuyamba bizinesi yao kapena ali kale pa bizinesi ndiye
akufuna kuyipititsa pa tsogolo. Maphunziro amenewa ama phunzitsidwa
mwa njira ya padera imene imalira inuyo kuti mudzichitira limodzi
ndi a phunzitsi (pulakitikolo). Maphunziro amenewa ndi opambana
chifukwa adayamba ndi a Jeremani ndipo ali kugwiritsidwa ntchito
ku maiko oposera 85.
Maphunziro
a CEFE anagawidwa mu zigawo zotsatirazi:
CEFE
woyamba: Ukachenjede wa Bizinesi Zoyenelera poyamba bizinesi
- Kudziwa moyo wa bizinesi
- Kumvetsa ndi kudziwa
luntha lako pa bizinesi
- Kupeza mathero a
moyo wako wa bizinesi
- Kukonzekera mfundo
zomkhwima pa bizinesi ndinso
- Kuphunzira kudziwa
mfundo zenizeni.
CEFE
wachiwiri: Dongosolo la Bizinesi
Dongosolo la bizinesi kuchokera m'maganizo ndi
kuyamba bizinesi yeniyeni
- Kudziwa zinthu zo
dzagulitsa pa bizinesi
- Kudziwa odzagula
- Kudziwa kapangidwe
ka zinthu
- Kudziwa odzagwira
ntchito
- Kudziwa ndalama zofunikira
ndinso
- Kuphunzira kalembedwe
ka dongosolo ya bizinesi (bizinesi pulani)
CEFE wachitatu :Kuchita
Bizinesi
- Kukonzetsa bizinesi
pulani
- Kudzigulitsa ndi
kugulitsa bizinesi
- Kopeza ndalama pa
bizinesi
- Kayankhulidwe ka
bizinesi ndinso
- Milandu pa bizinesi
Maphunzirowa amatenga
masiku 9 kuti umalize, CEFE 1 a metenga masiku 2, CEFE 2 a matenga
masiku 5 ndinso CEFE 3 a matenga masiku 2.
Pamene munthu amaliza
maphunziro amenewa amalandira satifiketi kusonyeza kuti wa landira
nzeru zoti akhoza ku chita bizinesi yopindulitsa.
|